PIC YAKHUTIRA NDI KATUNDU WOPANGIDWA NDI MAGULU A ANTHU  AULUMALI

Bungwe lothandiza kuphunzitsa anthu  kapangidwe kazinthu zosiyanasiyana la Project Innovation Center (PIC), lapereka chilolezo kumagulu a anthu aulumali  opanga zakumwa zopangidwa kuchokera kuzipatso m'boma la Dedza.Limozi mwa maguluwa ndi la Chisomo la m'muzi mwa Fosa m'dera la mfumu yaikulu (T/A) Kachere m'boma la Dedza kuti gululi lipitilize kupanga zakumwazi posaopa kuti zitha kubweretsa mavuto ena m'thupi la munthu.

Poyankhula pamene PIC imayeza katundu wopangidwa ndi anthuwa  kumalo oyezera zinthu (laboratory) kuchipatala cha Ntendere, komwe zotsatira zake zaonetsa kuti zakumwazi ziribe chiwopsezo pa moyo wa munthu, nkulu wa bungwe la PIC Kondwani Kachamba Ngwira wati achita izi kuti anthu akhulupilire kuti bungwe lawo limaphunzitsadi anthu kupanga zinthu mwaukadaulo ndi mwapamwamba.

"Bungwe lathu lidapatsidwa chilolezo ndi bungwe loyeza katundu la Malawi Beaural of Standards (MBS) ndipo mbiri yathu yabwino yapita patali kwambiri ndiyeno tidaganiza zobwera kuno kudzaonelera m'mene magulu a anthu aulumali omwe tidawaphunzitsa kapangidwe ka zinthu chaka chatha, kuti tione zinthu zomwe akupangazo kuti akuzipanga bwanji komanso kuona kuti  bizinezi zawo zikuyenda bwanji komanso koposaposa, tabwera  kudzawavomereza ngatidi akupanga zinthu zosapereka chiopsezo pa moyo wamunthu ndipo kuchokera mu kafukufuku yemwe tapeza poyeza katundu wawo, takhutira kuti akupanga katundu wopanda chiopsezo komanso wapamwamba", adatero Kachamba.

Kachamba waonjezenso kunena kuti PIC yalimbikitsika ndizomwe  anthu aulumali-wa akupangazi ndipo walimbikitsa anthuwa kuti alimbikire chifukwa zotere zipitisa patsogolo bizinezi zawo komano wapempha mabungwe ena kuthandizira anthuwa ndi mpamba kuti ntchito zamalonda zomwe akupanga zikwere.M'mawu ake, m'mozi mwa anthu aulumali omwe akupanga zakumwazi, Florida Kawache wati bungwe la PIC lawapatsa mangolomera  powaonjezera upangiri wakachitidwe ka businezi kotero izi zikulitsa ntchito zawo zamalonda.

Chaka chatha, Bungwe lomenyera ufulu wa anthu aulumali la FEDOMA mogwirizana ndi bungwe la Sightsavers kudzera mu project yosizidalira pachuma yomwe mabungwe awiriwa akupanga, mabungwewa adapempha bungwe la PIC kuti liphunzitse anthu aulumali m'maboma a Dedza ndi Machinga kapangidwe kazinthu zosiyanasiyana ndicholinga chofuna kutukula anthu aulumali-wa pantchito zamalonda.

Mabungwe atatuwa adapanga ulendo woyendera anthu aulumali-wa kuti  awone m'mene anthuwa akupangira zinthu zawo ndicholinga chofuna kuona ngati zinthu zomwe akupanga ziribe chiopsezo pamoyo wamunthu. 

Kupatula kupanga zakumwa, anthuwa akupanganso sopo, nkaka wopangidwa kuchokera kusoya, ndi zinthu zina zambiri ndipo magulu asanu ndi limozi am'boma la Dedza ndi omwe awalola kuti azipanga zinthu zapamwambazi zitaonetsa kuti ziribe vuto  kudzera mu zotsatira zomwe zatuluka kumalo oyezera zinthu.

Mabungwe a PIC, FEDOMA ndi Sightsavers adaphunzitsa anthu aulumali 80 ochita ntchito za malonda m'maboma a Dedza ndi Machinga ndipo uku kudali kuwayendera kuwapatsa chirimbikitso pazomwe ayamba kupanga.